Toptube Video Search Engine



Title:Thomas Chibade_MUKANDITAYIRE KUNYANJA (AUDIO)
Duration:05:40
Viewed:82,763
Published:11-06-2015
Source:Youtube

"Mukanditayire ku Nyanja" is a solid local reggae jive song released in 2005 by one of Malawi's popular musicians, THOMAS CHIBADE presents a vivid picture of domestic violence and advocates an end to it. LYRICS (ChiNyanja) (Chichewa): Abambowa 'samaone chonchi Akavala bwino ulemu poyenda Koma akaledzera mkazi ndi kapolo wawo Kumenya mkazi ngati mwina apha munthu Akaledzera amafuna nsima, ya ndiwo zankhulu komanso sanagule Akamabwera mkati mwa usiku, amayi amangolira: "zibhakera zikubwera" Ana kulira momvetsa chisoni, amayi akutuluka magazi mphuno ndi mkamwa Akumalira momvetsa chisoni mayi modandaula, kuganizira kwao "Amuna anga chonde!" Mukanditayire kunyanja Ndatopa, ndikapume Ndikamakufunsani chilungamo, mumandiyankha mwano, ndalakwanji ine? Anthu akwathuwa akundidabwa oh! chifukwa ndanyozeka Poti mwandivula ufumu wanga Banja ndikupilira koma ayi zina zinyanya Amayi asakachedwe kuchigayo, ku msika kapenanso ku mjigo Kothyola mnkhwani ngakhale kudondo Abambo amawatsatira konko Kuwachititsa manyazi pagulu Ngati nkuchigayo ufa onse kutaya pansi Kodi bambo mukamachita choncho, mumamva bwanji muli ndi mulongo wanu Mwamuna wake akumuchita choncho, inu okhala ankhoswe mungaweruze bwanji Kodi siuja kale munkangolira amayi anu akutibulidwa ndi mwamuna wao oh! Koma ngati ndi nkhanza zoyamwira, bambo adamwa tameki nanga mukaniranji? Musamatero choncho Bambo kutangwanidwa ndi wana kuntchito Tiwana take tosayenera kutero Kunama: "It's my office" mwina "Don't worry woman" But second see kuti ako ndi mwana Tiwana take small in appearance, teenager genuine but danger in actions Tikuchitira mwano mwini mwamuna, kulankhula motumbwa: "Nafenso tidya mommo" Mwanawe tamadzimvera chisoni, mDala uli nayo is same size with your father Akazi am'banja sizidole ngati akukwanani atayireni ena, akasiyanitse.... Mukanditayire kunyanja Ndatopa, ndikapume Ndikamakufunsani chilungamo, mumandiyankha mwano, ndalakwanji ine? Anthu akwathuwa akundidabwa oh! chifukwa ndanyozeka Poti mwandivula ufumu wanga Banja ndikupilira koma ayi zina zinyanya Ndi mwayi wanu bambo mwakwatira Musungane likhale banja la mtendere Anzanu afuna banja salipeza, awo! Angokwatira akazi aziwewe kale Othamanga, amwano, opanda mwambo Bambo ndipemphe chimodzi muleke nkhanza Amayi wanga musafere banja Kutchena ndi kukhwasula, mumtima ndi kapolo Nyimbo yanga siyothetsa mabanja Ine ndikungoimba nanunso mayi mumve poti... Akazi ena mumayerekedwa, mukaona mwamuma akukhalira pakwanu oh! Kusamva, makani ndi chisembwere, kusanduka mwamuna: "Kasake deya tidye", kulepheranso Zimakhala choncho, dziko lake lomweli Awo adali ndi mkazi wao, wa ulemu, womvetsa, wosunga mwambo Adawathawa chifukwa cha nkhanza zawo Zimakhala choncho, dziko lake lomweli Amayiwa adali ndi mwamuna wao, wolera, woveka, wodyetsa, womvetsa Adawathawa kaamba ka chisembwere



SHARE TO YOUR FRIENDS


Download Server 1


DOWNLOAD MP4

Download Server 2


DOWNLOAD MP4

Alternative Download :