Toptube Video Search EngineTitle:CRUISE 5 ELIYA NZERU WILLIAM
Duration:01:20:13
Viewed:360,075
Published:05-05-2021
Source:Youtube

Anthu ena amakhulupilira kuti ufiti kulibe - anthu amenewa sanakumane ndi a Eliya William. Iwe amatsimikiza kuti adatambako komanso adapangako using'anga. A Eliya anali mkulu wa bungwe la asing'anga ku Malawi kuyambila 1986 mpaka 1996. Iwo siabisa kuti achita zinthu zoopsya komanso aona zambiri kudzela mmatsenga. Iwo akutsindika kuti zambiri zimene timamva zokhudza amfiti ndizoona; amfiti amauluka kugwilitsa ntchito lichelo kapena tsache, ndondocha ndi anthu akufa amene amawathila mankhwala kuti achepe akatelo amawagwilitsa ntchito mmatsenga kuti azikaba ndalama kapena kulima kumunda, anthu amalodzana munjira zosiyanasiyana kuti wina afe kapena azikumana ndi matsoka. Nkhani yabwino ndiyakuti a Eliya zaufiti komanso using'anga adasiya ndipo pano adayamba kupemphela ku mpingo wa Zioni komwe adakwela mpaka kufika pa udindo wa Bishop.SHARE TO YOUR FRIENDS


Download Server 1


DOWNLOAD MP4

Download Server 2


DOWNLOAD MP4

Alternative Download :